Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 19:7-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Pamenepo Jonatani anaitana Davide, namuuza zonsezi. Ndipo Jonatani anafika naye Davide kwa Sauli, iye nakhalanso pamaso pace monga kale.

8. Ndipo kunalinso nkhondo; ndipo Davide anaturuka, nakamenyana ndi Afilisti, nawapha ndi maphedwe akuru, ndipo iwo anamthawa iye.

9. Ndipo mzimu woipa wocokera kwa Yehova unali pa Sauli, pakukhala iye m'nyumba mwace, ndi mkondo wace m'dzanja lace; ndipo Davide anayimba ndi dzanja lace.

10. Ndipo Sauli anayesa kupyoza Davide kumphatikiza kukhoma ndi mkondowo; koma iye anadzilanditsa kucoka pamaso pa Sauli; ndipo analasa khoma; ndipo Davide anathawa napulumuka usiku uja.

11. Ndipo Sauli anatumiza mithenga ku nyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa.

12. Comweco Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka.

13. Ndipo Mikala anatenga cifanizo naciika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwace, nacipfunda zopfunda.

14. Ndipo pamene Sauli anatumiza mithenga kuti ikamgwire Davide, anati, iye alikudwala.

15. Ndipo Sauli anatumiza mithengayo kuti ikaone Davide, nati, Mumtengere iye pa kama wace, kuti ndidzamuphe.

16. Ndipopakulowamithengayo, onani, pakama pali cifanizo ndi mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwace.

17. Nati Sauli kwa Mikala, Wandinyengeranii comweci, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Sauli, iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 19