19. Cifukwa cace Sauli anatumiza mithenga kwa Jese, nati, Vnditumizire Davide, mwana wako, amene ali kunkhosa.
20. Ndipo Jese anatenga buru namsenza mkate, ndi thumba la vinyo, ndi: mwana wa mbuzi, nazitumiza kwa Sauli ndi Davide mwana wace.
21. Ndipo Davide anafika kwa Sauli, naima pamaso pace; ndipo iye anamkonda kwambiri, namsandutsa wonyamula zida zace.
22. Ndipo Sauli anatumiza kwa Jese, nati, Ulole kuti Davide aime pamaso panga; pakuti ndamkomera mtima.
23. Ndipo kunali kuti pamene mzimu woipawo wocokera kwa Mulungu unali pa Sauli, Davide anatenga zeze, naliza ndi dzanja lace; comweco Sauli anatsitsimuka, nakhala bwino, ndi mzimu woipa unamcokeraiye.