Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 15:23-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Pakuti kupanduka kuli ngati coipa ca kucita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yacabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.

24. Ndipo Sauli anati kwa Samueli, Ndinacimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; cifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.

25. Cifukwa cace tsono, mukhululukire cimo langa, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova.

26. Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Ine sindibwerera nanu; pakuti munakaniza mau a Yehova, ndipo Yehova anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu ya Israyeli.

27. Ndipo pakupotoloka Samueli kuti acoke, iye anagwira cilezi ca mwinjiro wace, ndipo cinang'ambika.

28. Ndipo Samueli ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israyeli lero kuucotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.

29. Ndiponso Wamphamvu wa Israyeli sanama kapena kulapa; popeza iye sali munthu kuti akalapa.

30. Pomwepo iye anati, Ndinacimwa, koma mundicitire ulemu tsopano pamaso pa akuru a anthu anga, ndi pamaso pa Israyeli, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 15