Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 15:14-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo Samueli anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndirikumva m'makutu anga, ndi kulirako kwa ng'ombe ndirikumva, nciani?

15. Ndipo Sauli anati, Anazitenga kwa Aamaleki; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng'ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konse konse.

16. Pomwepo Samueli ananena ndi Sauli, Imani, ndidzakudziwitsani cimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.

17. Nati Samueli, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwa mutu wa mafuko a Israyeli? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israyeli,

18. Ndipo Yehova anakutumani ulendo, kuti, Muka, nuononge konse konse Aamaleki akucita zoipawo, nuponyane nao kufikira utawatha.

19. Cifukwa ninji tsono simunamvera mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova?

20. Ndipo Sauli ananena ndi Samueli, Koma ndinamvera mau a Yehova, ndipo ndinayenda njira Yehova anandituma ine, ndipo ndinabwera naye Agagi mfumu ya Amaleki, ndi Aamaleki ndinawaononga konse konse.

21. Koma anthuwo anatengako zowawanya, nkhosa ndi ng'ombe, zoposa za zija tidayenera kuziononga, kuziphera nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.

22. Ndipo Samueli anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kuchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo,

23. Pakuti kupanduka kuli ngati coipa ca kucita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yacabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.

24. Ndipo Sauli anati kwa Samueli, Ndinacimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; cifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.

25. Cifukwa cace tsono, mukhululukire cimo langa, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova.

26. Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Ine sindibwerera nanu; pakuti munakaniza mau a Yehova, ndipo Yehova anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu ya Israyeli.

27. Ndipo pakupotoloka Samueli kuti acoke, iye anagwira cilezi ca mwinjiro wace, ndipo cinang'ambika.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 15