Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 15:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo Samueli anadza kwa Sauli; ndipo Sauli anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinacita lamulo la Yehova.

14. Ndipo Samueli anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndirikumva m'makutu anga, ndi kulirako kwa ng'ombe ndirikumva, nciani?

15. Ndipo Sauli anati, Anazitenga kwa Aamaleki; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng'ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konse konse.

16. Pomwepo Samueli ananena ndi Sauli, Imani, ndidzakudziwitsani cimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.

17. Nati Samueli, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwa mutu wa mafuko a Israyeli? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israyeli,

18. Ndipo Yehova anakutumani ulendo, kuti, Muka, nuononge konse konse Aamaleki akucita zoipawo, nuponyane nao kufikira utawatha.

19. Cifukwa ninji tsono simunamvera mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova?

20. Ndipo Sauli ananena ndi Samueli, Koma ndinamvera mau a Yehova, ndipo ndinayenda njira Yehova anandituma ine, ndipo ndinabwera naye Agagi mfumu ya Amaleki, ndi Aamaleki ndinawaononga konse konse.

21. Koma anthuwo anatengako zowawanya, nkhosa ndi ng'ombe, zoposa za zija tidayenera kuziononga, kuziphera nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 15