Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 13:16-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo Sauli, ndi Jonatani mwana wace, ndi anthu akukhala nao anakhala ku Geba wa ku Benjamini; koma Afilistiwo anali nazo zithando zao ku Mikimasi.

17. Ndipo owawanya anaturuka ku zithando za Afilisti magulu atatu; gulu limodzi linalowa njira yonka ku Ofra, ku dera la Sauli;

18. gulu lina linalowa njira yonka ku Betihoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang'ana ku cigwa ca Zeboimu kucipululuko.

19. Ndipo m'dziko lonse la Israyeli simunapezeka wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisrayeli angadzisulire malupanga kapena mikondo;

20. koma Aisrayeli onse adafotsikira kwa Afilisti, kuti awasaniire munthu yense cikhasu cace, colimira cace, nkhwangwa yace, ndi khasu lace;

21. koma analf nao matupa kukonza makasu, ndi zikhasu ndi makasu a mana ndi nkhwangwazo; ndi kusongola zothwikira.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 13