Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 5:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israyeli, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wace ukulu wace unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israyeli, koma m'buku la cibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wace.

2. Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ace, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe);

3. ana a Rubeni mwana woyamba wa Israyeli: Hanoki, ndi Palu, Hezroni, ndi Karmi.

4. Ana a Yoeli: Semaya mwana wace, Gogi mwana wace, Simei mwana wace,

5. Mika mwana wace, Reaya mwana wace, Baala mwana wace,

6. Beera mwana wace, amene Tigilati Pilesere wa ku Asuri anamtenga ndende; ndiye kalonga wa Arubeni.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 5