Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 29:22-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. nadya namwa pamaso pa Mulungu tsiku lomwelo ndi cimwemwe cacikuru. Ndipo analonga ufumu Solomo mwana wa Davide kaciwiri, namdzozera Yehova akhale kalonga, ndi Zadoki akhale wansembe.

23. Momwemo Solomo anakhala pa mpando wacifumu wa Yehova, ndiye mfumu m'malo mwa Davide atate wace, nalemerera, nammvera iye Aisrayeli onse.

24. Ndi akuru onse, ndi amuna amphamvu onse, ndi ana amuna onse omwe a mfumu Davide, anagonjeratu kwa Solomo mfumu.

25. Ndipo Yehova anakuza Solomo kwakukuru pamaso pa Aisrayeli onse, nampatsa ulemerero wacifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israyeli inali nao wotero.

26. Momwemo Davide mwana wa Jese adakhala mfumu ya Aisrayeli onse.

27. Ndipo nthawi yoti anakhala mfumu ya Israyeli ndiyo zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu m'Hebroni, ndi zaka makumi atatu anakhala mfumu m'Yerusalemu.

28. Nafa atakalamba bwino, wocuruka masiku, zolemera, ndi ulemerero; ndi Solomo mwana wace anakhala mfumu m'malo mwaceo

29. Zocita mfumu Davide tsono, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Samueli mlauli, ndi m'buku la mau a Natani mneneri, ndi m'buku la mau a Gadi mlauli;

30. pamodzi ndi za ufumu wace wonse, ndi mphamvu yace, ndi za nthawizo zidampitira iye, ndi Israyeli, ndimaufumu onse a maiko.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 29