Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 29:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo mucita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikuru; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.

13. Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.

14. Kama ndine yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere? popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu.

15. Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.

16. Yehova Mulungu wathu, zounjikika izi zonse tazikonzeratu kukumangirani Inu nyumba ya dzina lanu loyera zifuma ku dzanja lanu, zonsezi ndi zanu.

17. Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Kama ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.

18. Yehova Mulungu wa Abrahamu, wa Isake, ndi wa Israyeli makolo athu, musungitse ici kosatha m'cilingaliro ca maganizo a mtima wa anthu anu, nimulunjikitse mitima yao kwanu,

19. nimupatse Solomo mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kucita izi zonse, ndi kumanga cinyumbaci cimene ndakonzeratu mirimo yace,

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 29