Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 27:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ana a Israyeli monga mwa ciwerengo cao, kunena za akuru a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu nchito iri yonse ya magawidwe, akulowa ndi kuturuka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya caka, cigawo ciri conse nca amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai.

2. Woyang'anira cigawo coyamba ca mwezi, woyamba ndiye Yasobeamu mwana wa Zabidiyeli; m'cigawo mwace munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.

3. Ndiye wa ana a Perezi, mkuru wa akazembe onse a khamu mwezi woyamba.

4. Woyang'anira cigawo ca mwezi waciwiri ndiye Dodai M-ahohi ndi cigawo cace; ndi Mikiloti mtsogoleri, ndi m'cigawo cace munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.

5. Kazembe wacitatu wa khamu wa mwezi wacitatu ndiye Benaya mwana wa Yehoyada wansembe wamkuru; ndi m'cigawo mwacemunalinso zikwi makumi awiri mphambu zinai.

6. Benaya ameneyo ndiye wamphamvu uja wa makumi atatu aja, woyang'anira makumi atatu aja; woyang'anira cigawo cace ndi Amizabadi mwana wace.

7. Wacinai wa mwezi wacinai ndiye Asebeli mbale wa Yoabu, ndi pambuyo pace Zebadiya mwana wace; ndi m'cigawo mwace munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.

8. Kazembe wacisanu wa mwezi wacisanu ndiye Samuti M-izra; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

9. Wacisanu ndi cimodzi wa mwezi wacisanu ndi cimodzi ndiye Ira mwana wa Ikesi Mtekoi; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

10. Wacisanu ndi ciwiri wa mwezi wacisanu ndi ciwiri ndiye Helezi Mpeloni wa ana a Efraimu; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

11. Wacisanu ndi citatu wa mwezi wacisanu ndi citatu ndiye Sibekai Mhusati wa Afera; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 27