Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 26:26-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Selomoti amene ndi abale ace anayang'anira cuma conse ca zinthu zopatulika, zimene Davide mfumu ndi akuru a nyumba za akulu, akuru a zikwi ndi mazana, adazipatula.

27. Kutenga pa zofunkha kunkhondo, anapatulako kukonzera nyumba ya Yehova.

28. Ndipo zonse adazipatula Samueli mlauli, ndi Sauli mwana wa Kisi, ndi Abineri mwana wa Neri, ndi Yoabu mwana wa Zeruya; ali yense anapatula kanthu kali konse, anazisunga Selomoti ndi abale ace.

29. A Aizara: Kenaniya ndi ana ace anacita nchito ya pabwalo ya Israyeli, akapitao ndi oweruza mirandu.

30. A Ahebroni: Hasabiya ndi abale ace odziwa mphamvu cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri anayang'anira Israyeli tsidya lino la Yordano kumadzulo, kuyang'anira nchito yonse ya Yehova, ndi kutumikira mfumu.

31. Yeriya ndiye mkuru wa Ahebroni, wa Ahebroni monga mwa mibadwo ya nyumba za makolo. Caka ca makumi anai ca ufumu wa Davide anafunafuna, napeza mwa iwowa ngwazi zamphamvu ku Yazeri wa ku Gileadi.

32. Ndi abale ace ngwazi ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri, akuru a nyumba za makolo, amene mfumu Davide anaika akhale oyang'anira a Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, pa zinthu zonse za Mulungu ndi zinthu za mfumu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 26