Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 22:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Tsono, mwana wanga, Yehova akhale nawe; nulemerere, numange nyumba ya Yehova Mulungu wako monga ananena za iwe.

12. Cokhaci, Yehova akupatse nzeru ndi luntha, nakulangize za Israyeli, kuti usunge cilamulo ca Yehova Mulungu wako,

13. Momwemo udzalemerera, ukasamalira kucita malemba ndi maweruzo amene Yehova analangiza Mose za Israyeli; limbikatu, nulimbike mtima, usaope, usade mtima.

14. Taona tsono, m'kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golidi, ndi matalente zikwi zikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, osayesa kulemera kwace, pakuti zidacurukaeli; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko.

15. Uli naonso anchito ocuruka ofukula miyala, ndi amisiri a miyala ndi a mitengo, ndi amuna onse aluso akucita nchito ziri zonse;

16. golidi, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, nzosawerengeka; nyamuka, nucite, Yehova akhale nawe.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 22