Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 20:3-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Naturutsanso anthu anali m'mwemo, nawaceka ndi mipeni ya mana mano, ndi zipangizo zocekera zacitsulo, ndi nkhwangwa. Anatero Davide ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwera ku Yerusalemu.

4. Ndipo zitatha izi, inauka nkhondo ku Gezeri ndi Afilisti; pamenepo Sibekai Mhusati anapha Sipai wa ana a cimphona; ndipo anawagonjetsa.

5. Ndipo panalinso nkhondo ndi Afgisti; ndi Elihanani mwana wa Yairi anapha Lami mbale wa Goliati Mgiti, amene luti la mkondo wace linanga mtanda woombera nsaru.

6. Ndipo panalinso nkhondo ku Gati; kumeneko kunali munthu wa msinkhu waukuru, amene zala zace za kumanja ndi kumapazi ndizo makumi awiri mphambu zinai; zisanu ndi cimodzi ku dzanja liri lonse, ndi zisanu ndi cimodzi ku phazi liri lonse; nayenso anabadwa mwa cimphonaco.

7. Ndipo potonza Israyeli iyeyu Yonatani mwana wa Simeya mbale wace wa Davide anamkantha.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 20