Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 20:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, pofikanso caka, nyengo yakuturuka mafumu, Yoabu anatsogolera khamu lamphamvu, napasula dziko la ana a Amoni, nadza, naumangira misasa Raba. Koma Davide anakhala ku Yerusalemu. Ndipo Yoabu anakantha Raba, naupasula.

2. Ndipo Davide anatenga korona wa mfumu yao kumcotsa pamutu pace, napeza kulemera kwace talente wa golidi; panalinso miyala ya mtengo wace pamenepo; ndipo anamuika pamutu pa Davide, naturutsa zankhondo za m'mudzimo zambiri ndithu.

3. Naturutsanso anthu anali m'mwemo, nawaceka ndi mipeni ya mana mano, ndi zipangizo zocekera zacitsulo, ndi nkhwangwa. Anatero Davide ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwera ku Yerusalemu.

4. Ndipo zitatha izi, inauka nkhondo ku Gezeri ndi Afilisti; pamenepo Sibekai Mhusati anapha Sipai wa ana a cimphona; ndipo anawagonjetsa.

5. Ndipo panalinso nkhondo ndi Afgisti; ndi Elihanani mwana wa Yairi anapha Lami mbale wa Goliati Mgiti, amene luti la mkondo wace linanga mtanda woombera nsaru.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 20