Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 18:11-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Izi zomwe mfumu Davide anazipatulira Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golidi adazitenga kwa amitundu onse, kwa Edomu, ndi kwa Moabu, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti, ndi kwa Amaleki.

12. Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu m'Cigwa ca Mcere zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.

13. Ndipo anaika asilikari a boma m'Edomu; ndi Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kuli konse anamukako.

14. Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisrayeli onse, naweruza anthu ace onse, nawacitira cilungamo.

15. Ndipo Yoabu mwana wa Zeruya anayang'anira khamu la nkhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri.

16. Ndi Zadoki mwana wa Ahitubu, ndi Abimeleki mwana wa Abyatara, anali ansembe, ndi Savisa anali mlembi,

17. ndi Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti; koma ana a Davide ndiwo oyamba ku dzanja la mfumu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 18