Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 18:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo zitatha izi, Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa, nalanda Gati ndi midzi yace m'manja a Afilisti.

2. Anakanthanso Moabu; ndi Amoabu anakhala anthu a Davide, nabwera nazo mphatso,

3. Ndipo Davide anakantha Hadarezeri mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wace ku mtsinje wa Firate.

4. Ndipo Davide analanda magareta ace cikwi cimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magareta, koma anasungako ofikira magareta zana limodzi.

5. Ndipo Aaramu a ku Damasiko anadza kudzathandiza Hadarezeri mfumu ya Zoba; koma Davide anakantha Aaramu amuna zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 18