Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 15:2-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira iye kosatha.

3. Ndipo Davide anasonkhanitsira Aisrayeli onse ku Yerusalemu, akwere nalo likasa la Yehova kumalo kwace adalikonzera.

4. Ndipo Davide anasonkhanitsa ana a Aroni ndi Alevi;

5. a ana a Kohati, Urieli mkuru wao, ndi abale ace zana limodzi mphambu makumi awiri;

6. a ana a Merari, Adaya mkuru wao, ndi abale ace mazana awiri mphambu makumi awiri;

7. a ana a Gerisomu, Yoeli mkuru wao, ndi abale ace zana limodzi mphambu makumi atatu;

8. a ana a Elizafana, Semaya mkuru wao, ndi abale ace mazana awiri;

9. a ana a Hebroni, Elieli mkuru wao, ndi abale ace makumi asanu ndi atatu;

10. a ana a Uzieli, Aminadabu mkuru wao, ndi abale ace zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.

11. Ndipo anaitana Zadoki ndi Abyatara ansembe, ndi Alevi Urieli, Asaya, ndi Yoeli, Semaya, ndi Elieli, ndi Aminadabu, nanena nao,

12. Inu ndinu akuru a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israyeli ku malo ndalikonzera.

13. Pakuti, cifukwa ca kusalinyamula inu poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anacita cotipasula, popeza sitinamfunafuma Iye monga mwa ciweruzo.

14. Momwemo ansembe ndi Alevi anadzipatula kuti akwere nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israyeli.

15. Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko ziri m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.

16. Ndipo Davide ananena ndi mkuru wa Alevi kuti aike abale ao oyimbawo ndi zoyimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi cimwemwe.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 15