Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 15:16-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo Davide ananena ndi mkuru wa Alevi kuti aike abale ao oyimbawo ndi zoyimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi cimwemwe.

17. Ndipo Alevi anaika Hemani mwana wa Yoeli, ndi a abale ace Asafu mwana wa Berekiya, ndi a ana a Merari, abale ao, Etani mwana wa Kusaya;

18. ndi pamodzi nao abale ao a kulongosola kwaciwiri, Zekariya, Beni, ndi Yaazieli, ndi Semiramoti, ndi Yehieli, ndi Uni, Bliabu, ndi Benaya, ndi Maaseya, ndi Matitiya, ndi Blifelehu, ndi Mikineya, ndi Obedi Bdomu, ndi Yeieli, ndikirawo.

19. Oyimba tsono: Hemani, Asafu, ndi Btani, anayimba ndi nsanje zamkuwa;

20. ndi Zekariya, ndi Azieli, ndi Semiramod, ndi Yehieli, ndi Uni, ndi Bliabu, ndi Maaseya, ndi Benaya, ndi zisakasa kuyimbira mwa Alimoti;

21. ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikeya, ndi Obedi Edomu, ndi Yeieli, ndi Azaziya, ndi azeze akuyimbira mwa Seminiti, kutsogolera mayimbidwe.

22. Ndi Kenaniya mkuru wa Alevi anayang'anira kusenzako; anawalangiza za kusenza, pakuti anali waluso.

23. Ndi Berekiya ndi Elikana anali odikira likasa.

24. Ndi Sebaniya, ndi Yosafati, ndi Netaneli, ndi Amasai, ndi Zekariya, ndi Benaya, ndi Eliezere, ansembe, analiza malipenga ku likasa la Mulungu; ndi Obedi Edomu ndi Yehiya anali odikira a likasa.

25. Momwemo Davide, ndi akuru akuru a Israyeli, ndi atsogoleri a zikwi, anamuka kukwera nalo likasa la cipangano la Yehova, kucokera ku nyumba ya Obedi Edomu mokondwera.

26. Ndipo popeza Mulungu anathandiza Alevi akusenza likasa la cipangano la Yehova, iwo anapha nsembe ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.

27. Ndipo Davide anabvala maraya abafuta, ndi Alevi onse akunyamula likasa, ndi oyimba, ndi Kenaniya woyang'anira kusenzaku, pamodzi ndi oyimba; Davide anabvalanso efodi wabafuta.

28. Momwemo Aisrayeli onse anakwera nalo likasa la cipangano la Yehova ndi kupfuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.

29. Ndipo polowa likasa la cipangano la Yehova m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli anasuzumira pazenera, naona mfumu Davide alikutumphatumpha ndi kusewera; ndipo anampeputsa mumtima mwace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 15