Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 14:11-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Atafika tsono ku Baala Perazimu, Davide anawakantha komweko; nati Davide, Mulungu anapasula adani anga ndi dzanja langa, ngati pokhamulira madzi. Cifukwa cace analicha dzina la malowo Baala Perazimu.

12. Ndipo anasiyako milungu yao; nalamula Davide, ndipo anaitentha ndi moto.

13. Ndipo Afilisti anabwerezanso, nafalikira m'cigwamo.

14. Ndipo Davide anafunsiranso kwa Mulungu, nanena Mulungu naye, Usakwera kuwatsata, uwazungulire, nuwadzere pandunji pa mitengo ya mkandankhuku.

15. Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula kunsonga kwa mitengo ya mkandankhuku, pamenepo uturukire kunkhondo; pakuti Mulungu waturukira pamaso pako kukantha gulu la Afilisti.

16. Nacita Davide monga Yehova adamuuza, nakantha gulu la Afilisti kuyambira ku Gibeoni kufikira ku Gezeri.

17. Ndipo mbiri ya Davide inabuka m'maiko onse, nafikitsira Yehova kuopsa kwace pa amitundu onse.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 14