Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 12:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. wacinai Misimana, wacisanu Yeremiya,

11. wacisanu ndi cimodzi Atai, wacisanu ndi ciwiri Elieli,

12. wacisanu ndi citatu Yohanani, wacisanu ndi cinai Elzabadi,

13. wakhumi Yeremiya, wakhumi ndi cimodzi Makibanai.

14. Awa a ana a Gadi, anali atsogoleri a nkhondo; wamng'ono wa iwo anayang'anira zana limodzi, ndi wamkuru wa iwo anayang'anira cikwi cimodzi.

15. Awa ndi omwe aja anaoloka Yordano mwezi woyamba, atadzala kusefukira magombe ace onse; nathawitsa onse okhala m'zigwa kum'mawa ndi kumadzulo.

16. Ndipo anadza ena a ana a Benjamini ndi Yuda kulinga kwa Davide.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 12