Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 10:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Momwemo anafa Sauli, ndi ana ace atatu; ndi nyumba yace yonse idafa pamodzi.

7. Ndipo pamene amuna onse a Israyeli okhala m'cigwamo anaona kuti anathawa, ndi kuti Sauli ndi ana ace adafa, anasiya midzi yao, nathawa; nadza Afilisti, nakhala m'menemo.

8. Ndipo m'mawa mwace anafika Afilisti kubvula za ophedwa, napeza Sauli ndi ana ace adagwa pa phiri la Giliboa.

9. Ndipo anambvula natenga mutu wace, ndi zida zace, natumiza ku dziko la Afilisti pozungulirapo, kulalika m'mafano ao ndi mwa anthu.

10. Ndipo anaika zida zace m'nyumba ya milungu yao, napacika mutu wace m'nyumba ya Dagoni.

11. Ndipo onse a Yabesi Gileadi, atamva zonse Afilisti adacitira Sauli,

12. anauka ngwazi zonse, nacotsa mtembo wa Sauli, ndi mitembo ya ana ace, nabwera nayo ku Yabesi, naika mafupa ao patsinde pa mtengo wathundu ku Yabesi, nasala masiku asanu ndi awiri.

13. Momwemo Sauli anafa, cifukwa ca kulakwa kwace analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunga; ndiponso cifukwa ca kufunsira wobwebweta, kufunsirako,

14. osafunsira kwa Yehova; cifukwa cace anamupha, napambutsira ufumu kwa Davide mwana wa Jese.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 10