Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 10:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndi nkhondoyi inamkulira Sauli, ndi amauta anampeza; ndipo anatenga nkhawa cifukwa ca amauta.

4. Pamenepo Sauli anati kwa wonyamula zida zace, Solola lupanga lako, nundipyoze nalo, angafike osadulidwa awa ndi kundiseka, Koma wonyamula zida zace anakana, popeza anaopa kwambiri. Pomwepo Sauli anatenga lupanga lace, naligwera.

5. Ndipo pamene wonyamula zida zace anaona kuti Sauli wafa, anagwera nayenso lupanga lace, nafa.

6. Momwemo anafa Sauli, ndi ana ace atatu; ndi nyumba yace yonse idafa pamodzi.

7. Ndipo pamene amuna onse a Israyeli okhala m'cigwamo anaona kuti anathawa, ndi kuti Sauli ndi ana ace adafa, anasiya midzi yao, nathawa; nadza Afilisti, nakhala m'menemo.

8. Ndipo m'mawa mwace anafika Afilisti kubvula za ophedwa, napeza Sauli ndi ana ace adagwa pa phiri la Giliboa.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 10