Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 6:17-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo nyumbayo, ndiyo Kacisi wa cakuno ca monenera, inali ya mikono makumi anai.

18. Ndipo m'kati mwa nyumba munali mikungudza yosemasema, ngati zikho ndi maluwa oti gada; munali mikungudza yokha yokha simunaoneka mwala ai,

19. Ndipo anakonza monenera m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwace, kuikamo likasa la cipangano la Yehova.

20. Ndipo m'kati mwa monenera m'menemo, m'litali mwace munali mikono makumi awiri, kupingasa kwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono makumi awiri; ndipo anamukuta ndi golidi woyengetsa, nakutanso guwa la nsembe ndi matabwa amkungudza,

21. Momwemo Solomo anakuta m'kati mwa nyumba ndi golidi woyengetsa, natambalika maunyolo agolidi cakuno ca monenera, namukuta ndi golidi.

22. Ndipo nyumba yonse anaikuta ndi golidi mpaka adatha nyumba yonse, ndi guwa lonse la nsembe linali cakuno ca monenera analikuta ndi golidi.

23. Ndipo m'moneneramo anasema mitengo yaazitona akerubi awiri, yense wa msinkhu wace mikono khumi.

24. Ndipo phiko limodzi la kerubi linali la mikono isanu, ndi phiko lina la kerubi linalinso la mikono isanu; kuyambira ku nsonga ya phiko limodzi kufikira ku nsonga ya phiko lina inali mikono khumi.

25. Ndi kerubi winayo msinkhu wace unali mikono khumi; akerubi onse awiri anafanana muyeso wao ndi msinkhu wao.

26. Msinkhu wa kerubi mmodzi unali mikono khumi, ndi wa kerubi wina momwemo.

27. Ndipo anaika akerubiwo m'cipinda ca m'katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lace la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba.

28. Ndipo anawakuta akerubi ndi golidi.

29. Nalemba m'makoma onse akuzinga cipinda mafano olemba ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, m'katimo ndi kumbuyo kwace.

30. Ndipo anakuta ndi golidi pansi pace pa nyumba m'katimo ndi kunja.

31. Ndipo pa khomo la monenera anapanga zitseko za mtengo waazitona, citando ca khomolo cinali limodzi la magawo asanu a khoma lace.

32. Zitseko ziwiri zomwe zinali za mtengo waazitona, anasemapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, nawakuta ndi golidi; inde anakutanso ndi golidi akerubi ndi migwalangwayo.

33. Momwemo anapanganso mphuthu zaazitona za pa khomo la Kacisi, citando cace cinali limodzi la magawo anai a khoma;

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 6