Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 4:2-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo akuru a mfumu ndi awa: Azariya mwana wa Zadoki anali nduna,

3. Elihorepa ndi Ahiya ana a Sisa alembi, Yehosafati mwana wa Ahiludi wolembera mbiri,

4. ndi Benaya mwana wa Yehoyada anali kazembe wa nkhondo, ndi Zadoki ndi Abyatara anali ansembe,

5. ndi Azariya mwana wa Natani anayang'anira akapitao, ndi Zabudi mwana wa Natani anali nduna yopangira mfumu,

6. ndi Ahisara anayang'anira banja la mfumu, ndi Adoniramu mwana wa Abida anali wamsonkho.

7. Ndipo Solomo anali nao akapitao khumi ndi awiri akuyang'anira Aisrayeli onse, akufikitsira mfumu ndi banja lace zakudya; ali yense anafikitsa zakudya zofikira mwezi umodzi wa caka.

8. Ndipo maina ao ndiwo: Benhuri anatengetsa ku mapiri a Efraimu;

9. Bendekeri ku Makazi ndi Saalibimu ndi Betsemesi ndi Elonibetanani;

10. Benhesedi ku Aruboti ndi Soko ndi dziko lonse la Heferi;

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 4