Ndipo Solomo anali nao akapitao khumi ndi awiri akuyang'anira Aisrayeli onse, akufikitsira mfumu ndi banja lace zakudya; ali yense anafikitsa zakudya zofikira mwezi umodzi wa caka.