Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 22:40-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. Ndipo Ahabu anagona ndi makolo ace; ndi Ahaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

41. Koma Yehosafati mwana wa Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda caka cacinai ca Ahabu mfumu ya Israyeli.

42. Yehosafati anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu, pamene analowa ufumu, nakhala nifumu zaka makumi awiri mphambu zisanu m'Yerusalemu. Ndi dzina la amace linali Azuba mwana wa Sili.

43. Ndipo anayenda m'njira yonse ya atate wace Asa, osapambukamo; nacita coyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaicotsa; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje.

44. Ndipo Yehosafati anacitana mtendere ndi mfumu ya Israyeli.

45. Tsono maciddwe ena a Yehosafati, ndi mphamvu anaionetsayo, ndi umo anathira nkhondo, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

46. Ndipo anacotsa m'dziko anyamata onyansa aja adatsalira masiku a atate wace Asa.

47. Ndipo m'Edomu munalibe mfumu, koma kazembe wa mfumu.

48. Yehosafati anamanga zombo za ku Tarsisi kukatenga golidi ku Ofiri; koma sizinamuka, popeza zinaphwanyika pa Ezioni Geberi.

49. Pamenepo Ahaziyamwana wa Ahabu ananena ndi Yehosafati, Anyamata anga amuke pamodzi ndi anyamata anu m'zombo. Koma Yehosafati anakana.

50. Ndipo Yehosafati anagona ndi makolo ace, naikidwa ndi makolo ace m'mudzi wa Davide kholo lace; ndipo Yoramu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

51. Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israyeli pa Samaria m'caka cakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri ca Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.

52. Nacita coipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wace, ndi ya amace, ndi ya Yerobiamu mwana wa Nebati, amene adacimwitsa Israyeli.

53. Natumikira Baala, namweramira, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli, monga umo anacitira atate wace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 22