Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 22:17-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Nati iye, Ndinaona Aisrayeli onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi ziribe mwini, yense abwerere ndi mtendere ku nyumba yace.

18. Pamenepo mfumu ya Israyeli inanena ndi Yehosafati, Kodi sindinakuuza kuti uyu sadzanenera za ine zabwino, koma zoipa?

19. Ndipo anati, Cifukwa cace tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wace wacifumu, ndi khamu lonse la Kumwamba liri ciriri m'mbali mwace, ku dzanja lamanja ndi lamanzere,

20. Nati Yehova, Adzanyenga Ahabu ndani, kuti akwere nagwe ku Ramoti Gileadi? Ndipo anati wina mwakuti, wina mwakuti.

21. Pamenepo mzimu wina unaturuka, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Nati Yehova kwa iye, Motani?

22. Nati, Ndidzaturuka, ndidzakhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ace onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; turuka, ukatero kumene.

23. Ndipo tsopano taonani, Yehova waika mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri anu onse awa, ndipo Yehova ananena coipa ca inu.

24. Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anasendera, napanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandicokera bwanji, kulankhula ndi iwe?

25. Mikaya nati, Taona, udzapenya tsiku lolowa iwe m'cipinda ca pakati kubisala.

26. Pamenepo inati mfumu ya Israyeli, Tengani Mikaya, mumbweze kwa Amoni kalonga wa mudzi, ndi kwa Yoasi mwana wa mfumu;

27. ndipo muziti, Itero mfumu, Khazikani uyu m'kaidi, mumdyetse cakudya ca nsautso, ndi madzi a nsautso, mpaka ndikabwera ndi mtendere.

28. Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhula mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.

29. Tsono mfumu ya Israyeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera ku Ramoti Gileadi.

30. Ndipo mfumu ya Israyeli inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulawa kunkhondo, koma bvala iwe zobvala zako zacifumu. Ndipo mfumu ya Israyeli inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo.

31. Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magareta ace, niti, Musaponyana ndi anthu ang'ono kapena akuru, koma ndi mfumu ya Israyeli yokha.

32. Ndipo kunali, akapitao a magareta ataona Yehosafati, anati, Zedi uyu ndiye mfumu ya Israyeli imene, napotolokera kukaponyana naye; koma Yehosafati anapfuula.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 22