26. Ndipo anacita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazicita Aamori, amene Yehova adawapitikitsa pamaso pa ana a Israyeli.
27. Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang'amba zobvala zace, nabvala ciguduli pathupi pace, nasala kudya, nagona paciguduli, nayenda nyang'anyang'a.
28. Pamenepo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati,
29. Waona umo wadzicepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzicepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa coipa cimeneci akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wace ndidzacifikitsa pa nyumba yace.