Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 17:16-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Mbiya ya ufa siidatha, ndi nsupa ya mafuta siinacepa, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya.

17. Ndipo kunali, zitatha izi, mwana wa mkazi mwini nyumbayo anadwala; ndipo pokula nthenda yace, analeka kupuma.

18. Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndiri nawe ciani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa chimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?

19. Ndipo ananena naye, Ndipatse mwana wako. Namtenga m'mfukato mwace napita naye ku cipinda cosanja cogonamo iyeyo; namgoneka pa kama wa iye mwini.

20. Napfuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, kodi mwamgwetsera coipa mkazi wamasiye amene ndikhala naye, kumphera mwanace?

21. Nafungatira katatu pa mwanayo, napfuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, ndikupemphanf, ubwere moyo wace wa mwanayu m'cifuwa mwace.

22. Ndipo Yehova anamvamau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo.

23. Ndipo Eliya ananyamula mwanayo, natsika naye ku cipinda cosanja, nalowa naye m'nyumba, nampereka kwa amace; nati Eliya, Taona, mwana wako ali moyo.

24. Ndipo mkazi anati kwa Eliya, Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mau a Yehova ali m'kamwa mwanuwo ngoona.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 17