14. Popeza atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzacepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova pa dziko lapansi.
15. Ndipo iye anakacita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m'nyumba ace, masiku ambiri.
16. Mbiya ya ufa siidatha, ndi nsupa ya mafuta siinacepa, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya.
17. Ndipo kunali, zitatha izi, mwana wa mkazi mwini nyumbayo anadwala; ndipo pokula nthenda yace, analeka kupuma.