Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 15:7-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo macitidwe ace ena a Abiya, ndi zonse anazicita, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobiamu.

8. Nagona Abiya ndi makolo ace, namuika anthu m'mudzi wa Davide; Asa mwana wace nalowa ufumu m'malo mwace.

9. Ndipo caka ca makumi awiri ca Yerobiamu mfumu ya Israyeli, Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda.

10. Nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai mphambu cimodzi, ndipo dzina la amace linali Maaka mwana wa Abisalomu.

11. Ndipo Asa anacita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lace.

12. Nacotsa m'dziko anyamata aja adama, nacotsanso mafano onse anawapanga atate ace.

13. Ndipo anamcotsera Maaka amace ulemu wa mace wa mfumu, popeza iye anapanga fano lonyansitsa likhale cifanizo; ndipo Asa analikha fano lace, nalitentha ku mtsinje wa Kidroni.

14. Koma misanje sanaicotsa, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ace onse.

15. Ndipo analonga m'nyumba ya Yehova zinthu zija atate wace adazipereka; napereka zinthu zina iye mwini zasiliva ndi zagolidi ndi zotengera.

16. Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Basa mfumu ya Israyeli masiku ao onse.

17. Ndipo Basa mfumu ya Israyeli anakwera ndi nkhondo ku Yuda, namanga ku Rama kuwaletsa anthu asaturuke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.

18. Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golidi yense anatsala pa cuma ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ciri m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ace; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabrimoni, mwana wa Hezroni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 15