Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 15:32-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Basa mfumu ya Israyeli masiku ao onse.

33. Tsono Basa mwana wa Ahiya analowa ufumu wa Israyeli caka cacitatu ca Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ku Tiriza zaka makomi awiri mphambu zinai.

34. Ndipo anacimwa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya Yerobiamu, ndi m'chimo lace iye anacimwitsa nalo Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 15