Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 14:19-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo macitidwe ena a Yerobiamu m'mene umo anacitira nkhondo, ndi m'mene umo anacitira ufumu, taona, analembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

20. Ndipo masiku akukhala Yerobiamu mfumu anali zaka makumi awiri mphambu ziwiri, nagona iye kwa makolo ace, nalowa ufumu m'malo mwace Nadabu mwana wace.

21. Ndipo Rehabiamu mwana wa Solomo anali mfumu ya dziko la Yuda. Rehabiamu anali wa zaka makumi anai mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, m'mudzi m'mene Yehova adausankha m'mafuko onse a Israyeli kukhazikamo dzina lace. Ndipo dzina la amace linali Naama M-amoni.

22. Ndipo Ayuda anacita zoipa pamaso pa Yehova, namcititsa nsanje ndi zoipa zao anazicitazo, zakuposa zija adazicita makolo ao,

23. Pakuti anadzimangiranso misanje, ndi zoimiritsa, ndi zifanizo, pa citunda conse cacitali, ndi patsinde pa mtengo wogudira uli wonse;

24. panalinso anyamata ocitirana dama m'dzikomo; iwo amacita monga mwa zonyansitsa za amitundu, amene Yehova anapitikitsa pamaso pa ana a Israyeli.

25. Ndipo kunacitika, Rebabiamu atakhala mfumu zaka zisanu, Sisaki mfumu ya Aigupto anakwera ndi nkhondo ku Yerusalemu,

26. nacotsa cuma ca m'nyumba ya Yehova, ndi cuma ca m'nyumba ya mfumu; inde anacotsa conseco, nacotsanso zikopa zagolidi zonse adazipanga Solomo.

27. Ndipo mfumu Rehabiamu anapanga m'malo mwa izo zikopa zina zamkuwa, nazipereka m'manja a akapitao a olindirira, akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.

28. Ndipo kunacitika, pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, olindirira aja anazinyamula, nabweranso nazo ku cipinda ca olindirirawo.

29. Tsono, macitidwe ace ena a Rehabiamu, ndi zonse anazicita, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

30. Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehabiamu ndi Yerobiamu masiku ao onse.

31. Nagona Rehabiamu ndi makolo ace, naikidwa kwa makolo ace m'mudzi wa Davide. Ndipo dzina la amace linali Naama M-amoni, nalowa ufumu m'malo mwace Abiya mwana wace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 14