Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 14:11-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Agaru adzadya ali yense wa Yerobiamu wakufa m'mudzi; ndi mbalame za m'mlengalenga zidzadya yense wakufera kuthengo; popeza wanena ndi Yehova.

12. Tanyamuka tsono, numuke kwanu; pakulowa mapazi ako m'mudzi mwanayo adzatsirizika.

13. Ndipo Aisrayeli onse adzamlira, nadzamuika, popeza iye yekha wa ana a Yerobiamu adzalowa m'manda; pakuti mwa iye mwapezedwa cokoma ca kwa Yehova Mulungu wa Israyeli m'nyumba ya Yerobiamu.

14. Ndiponso Yehova adzadziukitsira mfumu ya Israyeli, idzaononga nyumba ya Yerobiamu tsiku lomwelo; nciani ngakhale tsopano apa?

15. Popeza Yehova adzawakantha Aisrayeli monga bango ligwedezeka ndi madzi, nadzazula Aisrayeli m'dziko lino labwino analipatsa makolo ao, nadzawamwazira ku tsidya lija la Firate, popeza iwo anapanga zifanizo zao zokwiyitsa Yehova.

16. Ndipo adzai pereka Aisrayeli cifukwa ca macimo a Yerobiamu anacimwawo, nacimwitsa nao Aisrayeli.

17. Ndipo mkazi wa Yerobiamu ananyamuka nacoka, nafika ku Tiriza; ndipo polowa iye pa khomo la nyumba yace anatsirizika mwanayo.

18. Ndipo anamuika, namlira Aisrayeli, monga mwa mau a Yehova anawalankhula pa dzanja la mtumiki wace Ahiya mneneri.

19. Ndipo macitidwe ena a Yerobiamu m'mene umo anacitira nkhondo, ndi m'mene umo anacitira ufumu, taona, analembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

20. Ndipo masiku akukhala Yerobiamu mfumu anali zaka makumi awiri mphambu ziwiri, nagona iye kwa makolo ace, nalowa ufumu m'malo mwace Nadabu mwana wace.

21. Ndipo Rehabiamu mwana wa Solomo anali mfumu ya dziko la Yuda. Rehabiamu anali wa zaka makumi anai mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, m'mudzi m'mene Yehova adausankha m'mafuko onse a Israyeli kukhazikamo dzina lace. Ndipo dzina la amace linali Naama M-amoni.

22. Ndipo Ayuda anacita zoipa pamaso pa Yehova, namcititsa nsanje ndi zoipa zao anazicitazo, zakuposa zija adazicita makolo ao,

23. Pakuti anadzimangiranso misanje, ndi zoimiritsa, ndi zifanizo, pa citunda conse cacitali, ndi patsinde pa mtengo wogudira uli wonse;

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 14