Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 13:30-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Ndipo mtembo wace anauika m'manda a iye mwini, namlira iwo maliro, nati, Mayo, mbale wanga!

31. Ndipo kunacitika, atamuika iye, ananena ndi ana ace, nati, Nkadzamwalira ine mudzandiike ine m'manda momwemo mwaikidwa munthu wa Mulunguyo, ikani mafupa anga pafupi ndi mafupa ace.

32. Popeza mau aja anawapfuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe la ku Beteli, ndi kutemberera nyumba zonse za misanje iri m'midzi ya ku Samariya, adzacitika ndithu.

33. Pambuyo pa ici Yerobiamu sanabwerera pa njira yace yoipa, koma analonganso anthu acabe akhale ansembe a misanje, yensewakufuna yemweyu anampatula akhale wansembe wa misanje,

34. Ndimo umu munali chimo la nyumba ya Yerobiamu, limene linaidula ndi kuiononga pa dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 13