Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 11:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mfumu Solomo anakonda akazi ambiri acilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Moabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Zidoni, ndi Ahiti;

2. a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israyeli za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomo anawaumirira kuwakonda.

3. Ndipo anali nao akazi mazana asanu ndi awiri, ana akazi a mafumu, ndi akazi acabe mazana atatu; ndipo akazi ace anapambutsa mtima wace.

4. Ndipo kunali, atakalamba Solomo, akazi ace anapambutsa mtima wace atsate milungu yina; ndipo mtima wace sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wace monga mtima wa Davide atate wace.

5. Tsono Solomo anatsata Asitoreti fano la anthu a Zidoni, ndi Milikomu fano lonyansitsa la Aamoni.

6. Ndipo Solomo anacita coipa pamaso pa Yehova, osatsata Yehova ndi mtima wonse monga Davide atate wace.

7. Pamenepo Salomo anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amoabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, pa phiri liri patsogolo pa Yerusalemu.

8. Ndipo momwemo anacitiranso akazi ace onse acilendo, amene amafukizira naphera nsembe mafano ao.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 11