Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 1:45-50 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

45. Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri anamdzoza mfumu ku Gihoni, ndipo acokera kwneneko cikondwerere, ndi m'mudzimo muli phokoso. Ndilo phokoso limene mwamvali.

46. Ndiponso Solomo wakhala pa cimpando ca ufumu.

47. Ndiponso akapolo a mfumu anadzadalitsa Davide mbuye wathu mfumu, nati, Mulungu wanu aposetse dzina la Solomo lipunde dzina lanu, nakulitse mpando wace wacifumu upose mpando wanu wacifumu; ndipo mfumu anawerama pakamapo.

48. Ndiponso watero mfumu, Wolemekezeka Yehova Mulungu wa Israyeli, amene wapereka lero wina wokhala pa mpando wanga wacifumu, maso anga ali cipenyere.

49. Pamenepo oitanidwa onse a Adoniya anacita mantha, nanyamuka, napita yense njira yace.

50. Ndipo Adoniya anaopa cifukwa ca Solomo, nanyamuka, nakagwira nyanga za guwa la nsembe.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 1