46. ]
47. Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe m'Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa m'gehena;
48. kumeneko mphutsi yao siikufa, ndi mota suzimidwa.
49. Pakuti onse adzathiridwa mcere wamoto,
50. Mcere uli wabwino; koma ngati mcere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi ciani? Khalani nao mcere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzace.