6. Ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasoceretsa ambiri.
7. Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zace za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenerakucitika izi; koma sicinafike cimariziro.
8. Pakuti mtundu wa anthu udzayambana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu unzace: padzakhaia zibvomezi m'malo m'malo; padzakhala njala; izi ndi zoyambira za zowawa.
9. Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akuru a mirandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafwnu mudzaimirira cifukwa ca Ine, kukhale umboni kwa iwo.
10. Ndipo Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.
11. Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musada nkhawa usanayambe mrandu ndi cimene mudzalankhula; koma ci mene cidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, mucilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.