40. Koma Petro anawaturutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ace; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.
41. Ndipo Petro anamgwiradzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.
42. Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye.
43. Ndipo kunali, kuti anakhala iye m'Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.