1. Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza akuphunzira ena;
2. ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupira? Ndipo anati, lai, sitinamva konsekuti Mzimu Woyera waperekedwa.
3. Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m'ciani? Ndipo anai, Mu ubatizo wa Yohane.