1. Ndipo anafikanso ku Derbe ndi Lustra; ndipo taonani, panali wophunzira wina pamenepo, dzina lace Timoteo, amace ndiye Myuda wokhulupira; koma atate wace ndiye Mhelene.
2. Ameneyo anamcitira umboni wabwino abale a ku Lustra ndi Ikoniyo.
3. Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, cifukwa ca Ayuda amene anakhala m'maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wace anali Mhelene.
4. Pamene anapita kupyola pamidzi, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamulira atumwi ndi akuru a pa Yerusalemu.
5. Kotero Mipingoyo inalimbikitsidwa m'cikhulupiriro, nacuruka m'ciwerengo cao tsiku ndi tsiku.
6. Ndipo anapita pa dziko la Frugiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau m'Asiya; pamene anafika kundunji kwa Musiya,
7. anayesa kunka ku Bituniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza;
8. ndipo pamene anapita pambali pa Musiya, anatsikira ku Trowa.
9. Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Makedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Makedoniya kuno, mudzatithangate ife.