26. Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! pakuti makolo ao anawatero momwemo ananeri onama.
27. Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; citirani zabwino iwo akuda inu,
28. dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akucitira inu cipongwe.
29. Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzace; ndi iye amene alanda copfunda cako, usamkanize malaya ako.
30. Munthu ali yense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso.
31. Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakucitirani inu, muwacitire iwo motero inu momwe.