Ndipo ananena kwa ilo kuti lisaipse udzu wa padziko, kapena cabiriwiri ciri conse, kapena mtengo uli wonse, koma anthu amene alibe cizindikilo ca Mulungu pamphumi pao ndiwo.