Ndipo Iye wakukhala pa mpando wacifumu anati, Taonani, ndicita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mau awa ali okhulupirika ndi oona.