Ndipo anatsegulidwa Kacisi wa Mulungu amene ali m'Mwamba; ndipo linaoneka likasa la cipangano cace, m'Kacisi mwace, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi cibvomezi, ndi matalala akuru.