14. nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kucurukitsa ndidzakucurukitsa iwe.
15. Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo.
16. Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'citsutsano cao ciri conse lumbiro litsiriza kutsimikiza.
17. Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mocurukira kwa olowa a lonjezano kuti cifuniro cace sicisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;
18. kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale naco coticenjeza colimba, ife amene tidathawira kucigwira ciyembekezo coikika pamaso pathu;
19. cimene tiri naco ngati nangula wa moyo, cokhazikika ndi colimbanso, ndi cakulowa m'katikati mwa cophimba;
20. m'mene Yesu mtsogoleri analowamo cifukwa ca ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.