16. ena atero ndi cikondi, podziwa kuti anandiika ndicite eokanira ca Uthenga Wabwino;
17. koma ena alalikira Kristu mocokera m'cotetana, kosati koona, akuyesa kuti adzandibukitsira cisautso m'zomangira zanga.
18. Potero nciani? Cokhaco kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m'coonadi, Kristu alalikidwa; ndipo m'menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera.
19. Pakuti ndidziwa kuti ici cidzandicitira ine cipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Kristu;
20. monga mwa kulingiriritsa ndi ciyembekezo canga, kuti palibe cinthu cidzandicititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Kristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwamoyo, kapena mwa imfa.