18. Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu.
19. Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.
20. Pakuti ufumu wa Mulungu suli m'mau, koma mumphamvu, Mufuna ciani?
21. Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwacikondi, ndi mzimu wakufatsa?