Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu a'khungu, popeza anacimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati pfumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.